27/12/2025
Mauthenga achisoni akupitilira kuperekedwa kutsatira imfa ya aluso asanu omwe afa pa ngozi ya galimoto dzulo.
Oyimba komanso anthu osiyanasiyana alemba mauthenga awo achisoni pamatsamba awo amchezo kusonyezo kukhudzika kwawo ndi imfayi.
Ena mwa aluso komanso oimba omwe apereka mauthenga awo ndi monga Lulu, Gwamba, Driemo, Steve Muliya, Tuno komanso Robert Chiwamba.
Pakadali pano chipani cha UTM kudzera mu kalata yomwe chatulusa chati ndichokhudzika ndi imfayi.
Icho chati alusowa amatenga nawo gawo polimbikitsa chikhalidwe komanso posangalatsa anthu m'dziko muno.
-Joseph Mphiya-