Uthenga Wachitsitsimutso M'matsiku Otsiliza

Directions

Uthenga Wachitsitsimutso M'matsiku Otsiliza Uthenga Wachitsitsimutso M'matsiku Otsiliza

17/07/2026

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO MASIKU OTSILIZA

𝗠𝗔𝗨 𝗢𝗗𝗭𝗨𝗞𝗜𝗥𝗔

" Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka."

AGALATIYA 6:9

Okondedwa, kuchitira ena zabwino ndi madalitso chifukwa amabwenzera ndi mwini wake Mulungu, ndi chifukwa tikuyenera kuti tisaleme.

Mukhale ndi tsiku lopambana.
𝗔𝗺𝗲𝗻.

14/06/2026

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA.

MAU OGONERA:

Nati,kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.
¹⁵ Ndipo potero atapilira analandira lonjezanolo.
AHEBRI 6 :14-

Mulungu ndi wachifundo ndipo ndi wa chikondi koma madalitso enawa amadikila tichite mbali yathu, ndife okhulupilika kulandira m'dalitso wake,?

■Kodi ndife opilira kuti Ambuye atatidalitsa tizathandidzanso am'nzathu ena osowa osati mowatonza koma mowapatsa ndi mn'tima wathu onse ?

■Tisataye m'ntima Mulungu ndi wa nthawi tikhale opilira ndipo tidikile nthawi ya Ambuye

Mukhale ndi Usiku Wabwino Mulungu Akudalitseni.
📖🎺🎺

13/06/2026

🌿 UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA 🌿

"Koma inu mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzabwera pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga." (Machitidwe 1:8)

Mulungu amatipatsa mphamvu kudzera mwa Mzimu Woyera kuti tikhale mboni zake kulikonse komwe tili. Musalole zovuta za moyo kukufooketsani, chifukwa Mulungu ali nanu ndipo adzakulimbitsani tsiku lililonse.

🙏 Pemphero: Ambuye, ndipatse mphamvu ndi nzeru kuti ndiyende m'njira zanu ndi kukhala mboni yabwino ya Ufumu wanu. Amen.

Mukhale Ndi Usiku wabwino Nonse Ambuye Atiyang'anire Amen.

09/06/2026

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA.

Lingaliro la Kadzutsa

✍️9/6/26
Mukachita mantha, mugwa gadaa!

📚 Neh. 6:1-19
13. Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza.*

14. Mukumbukile, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa nchito zao izi... amene anafuna kundiopsa.

Akatswiri ophunzira za makhalidwe a nyama (animal behaviorists) anatsimikiza kuti anthu a mantha ali pa chiopsezo chachikulu chojiwa ndi zirombo zakuthengo kuposa anthu opanda mantha.

Mundime yathu lero, adani.a Ayuda alephera kusokoneza ntchito yomanga malinga kufikira yatha. Tsopano akufuna kumugwetsa mphwayi Nehemiya pomuopsa. Koma Nehemiya sakutekeseka!

Lero muuzeni Ambuye akugwirizizeni musatekeseke poopsedwa ndi mdani. AMEN.

"Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso." (2 Tim. 1:7)

Mukhale ndi tsiku lopambana.

08/06/2026

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA.

Ndife odala

Ndipo M'mene anapotolokera kwa ophunzira ake, ali pa okha, anati, odala masowo akuona zimene muona.
²⁴ Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu mudziona,koma sanadziona: ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimva.
LUKA 10 :23 -
Uthenga wa chipulumutso walarikidwa kwa mitundu yonse, zilankhulidwe zonse. Ndipo ngati titalephera kupulumuka Ambuye akudalitseni

mukhale ndi tsiku lopambana. 📖🎺🎺

12/03/2026

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MASIKU OTSIZA.

MAU ODZUKILA

Udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu. 8, Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.

YESAYA 40:7-8📖🛌
Mau a Mulungu adzakhala kwa nthawi zonse, ndipo sanakhalepo wonama, sanakhalepo wopanda pake, chifukwa wodikira Mulungu sadikira ulele.

Mukhale ndi tsiku Lopambana nonse Amen.

02/01/2026

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA.

MAU WODZUKIRA MORNING WATCH

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, ndiwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

YAKOBO 1:5📖🛏️
Mu 2026 tiyeni tifunsire nzeru kwa Mulungu, tipemphe amapereka mosaona nkhope, mosaona mmene munthu akuonekera dalirani kwa Mulungu.
Chaka chabwino kwa nonse Mulungu akhale patsogolo nthawi zonse

09/12/2025

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA

MAU OGONERA!!!

Kafukufuku pa dziko lapansi amaonetsa kt aliynse amafuna kuwala usku ngakhale usana. Iz ndayankhula chfk chakt... poyamba magetsi anali m'matauni mokha kma lero even kumudz anthu agula ma solar kupanga wirering kuika ma bulb m'nyumba kumawala ndthu. Iz ndapeza kt palibe yemwe amasangalala nd mdima.

Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi ( CHIBVUMBULUTSO 22:5).

Abwenzi, nthaw yomwe takhala pa dziko lapansi pano ambiri takhala tikuduliridwa magetsi chfk chosalipira ma bill a magetsi. Lero ngakhale kuli magetsi a ma units wena tkulepherabe kugula magetsi. Kma nkhani yosangalatsa nayi...tkadzapulumutsidwa kupita kumwamba sitidzafunanso kuwala kwa magetsi, nyali or dzuwa uski nd usana. Chfk ulemerero wa Yesu Khristu mwini udzakhala ukutiunikira.
Abwenzi, titalingalira mozama dzko lapansi losautsali anthu tkukanika kugula magetsi a 500 MK. Ndye kumwamba kuwala kukakhala kwa ulele bola tikachita bwno pansi pano maka posiya machimo athu. Madzulo ano ndmati ndikuitaniren kuulendo opita kumwamba tkaone olemelero nd kuwala kwa Yesu Khristu yemwe takhala tkumulindira.
Okondedwa, tikachita bwno kupita kumwamba sitikaona kuwala kokha ayi. Tikaonanso Eliya nd Enoch omwe adapita ali amoyo. Potha pa zonse tidzachita ufumu nd Yesu Khristu kwa chaka chikwi ( 1,000 yrz.

MUKHALE NDI USIKU WABWNO MULUNGU AKUSUNGENI AMEN 🙏

TANGOOTCHANI MTENGOWO BASIMmudzi wina munamveka mau  akuti njoka🗣, njoka🗣, ndipo anthu onse anathamanga ndizida mmanja k...
21/11/2025

TANGOOTCHANI MTENGOWO BASI

Mmudzi wina munamveka mau akuti njoka🗣, njoka🗣, ndipo anthu onse anathamanga ndizida mmanja kuti akaphe njokayo.
Azimai anatenga misi, azibambo anatenga zikwanje, mauta ena zibonga kuti akaphe njokayo.

Chinali chinjoka chachikulu🐍, koma chitaona anthu, icho chinathawira mu mphanga ya mtengo omwe unali pafupi kwambiri ndinyumba ya amfumu 🌳🏠. Anthu anayesetsa kuti aiphe koma zinalephera.

Amfumu atamva izi anakana kuti chilombocho achisiye chilindimoyo mumtengo omwe ulipakhomo pawo, ndipo analamula kuti mtengowo uwotchedwe 🔥 ndipo zinachitikadi.

🥦FUNSO🥦?
Unalakwanji mtengo kuti uwotchedwe🤷‍♀?
Ngati mukuganiza kuti nchifukwa choti unasunga mphanga yomwe munalowa njoka🐍, zikomo kwambiri.

🥦PHUNZIRO🥦.
Njoka ndiye satana, mtengo ndife wanthu ndipo mphanga ndiwo mtima wathu, pamene mfumu ndiye Mulungu.

Tikuyenera kusamala kwambiri, chifukwa tikampatsa satana kulowa mumtima mwathu ife tidzaonongedwa monga zinakhalira ndi mtengo uja. Cholinga cha Mulungu ndikudzaononga tchimo padziko lino lapansi, koma tikalisunga tchimolo mumtima mwathu, ndithu tidzaonongedwa mwai opulumuka ulimmanja mwathu

Ambuye Akudalitseni Nonse Mukhale Ndi Tsiku lopambana.

09/11/2025

UTHENGA WACHITSITSIMUTSO M'MATSIKU OTSILIZA

MAU OGONERA :

Mutidziwitse kuwelenga masiku athu motero,
Kuti tikhale nao m'tima wa nzeru.
MASALIMO 90 : 12

■ Okondedwa, Mulungu anatipatsa nzeru ndipo tilinawo aluso pakati pathu dziko limawadalira iwo akakhapo.

■ Ngakhale alusowa ndi anzeruwa alipo koma M'mawa lawo salidziwa chifukwa liri m'dzanja la Yehova.

■ Wolemela, wosauka, wotchuka wopanda m'funda wopanda kanthu,tonse timagona tulo ndipo sitimadziwa kanthu mkati mwa tulo tathu.

■ Alipo M'modzi yekha Yehova amene amapatsa mneru chidziwitso ngakhale chuma.
■Tidalire pa Yehova ndipo akhale oyamba, amene amadziwa za m'mawa lathu.
Mukhale ndi usiku opambana Amen Amen.

Address

Benoni

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Uthenga Wachitsitsimutso M'matsiku Otsiliza posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share