
08/08/2025
ZINA MWA NKHANI ZIKULUZIKULU ZOMWE ZINALIKO DZULO
1️⃣ A David Mbewe omwe dzulo auzidwa ndi bungwe la MEC kuti sakuyenela kupikitsana nawo pa mpando wau president, chifukwa zowayeneleza nzotsakwanila, apanga alliance ndi chipani cha DPP.
2️⃣ Nduna ya za maboma ang’onoang'ono, a Richard Chimwendo Banda, akweza mafumu 7 m'boma la Nkhata Bay. Ena mwa Mafumuwa ndi a senior chief Nyaliwanga ndi M’bwana omwe achoka pa u T/A, a T/A Thula kuchoka pa Sub T/A ndipo a sub T/A Mkondowe Chiweyo, Kamwadi ndi Mbalambala, akwezedwa kuchoka pa ugulupu.
3️⃣ Unduna wa za malo wati wakwanitsa kumanga nyumba pafupifupi 67 za anthu akhungu lachi alubino m'dziko muno.
4️⃣ Kampane ya Ekhaya, yapeleka ndalama zokwana K12 million kwacha ku phwando la maimbidwe lomwe Praise Umali akukonza. Ndalamayi ndi yoti ithanzizile Zina ndi Zina zokonzekera phwandoli.
5️⃣ Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) laimitsa ntchito yopereka mafuta agalimoto kukampani ya SIMSO Oil and Transport kaamba kopezeka ikusunga mafuta agalimoto oposa malita 200,000 opanda chifukwa.
6️⃣ A police ku Masambaanjati m'boma la Thyolo asimikiza kuti amanga wamsembe wa mongo wa Catholic a Daniel Makwiti apa Konzaalendo Parish powaganizira kuti anagwirilira ndikumpasa mimba mwana wa zaka 16 yemwe anali standard 7.
7️⃣ Apolisi pa Masuku m'boma la Mangochi amanga a Alfred Alli Malinga a zaka 27, chifukwa chowaganizira kuti apezeka ndi mafuta a Petulo okwana malita 550 popanda chilolezo.
8️⃣ A police m'boma la Mwanza amanga a Beauty Limbe komanso a Grace Marting chifukwa chopezeka ndi mafuta pafupifupi 30 litres omwe amagulitsa opanda chilolezo.
9️⃣ Apolisi m'boma la Salima amanga a Davison Mphande azaka 29 powaganizila kuti anagwililira mwana wawo omupeza wazaka 11.
🔟 Katswiri osewera mpira wa miyendo wa zimayi Temwa TC6 Chawinga, yemwe amaseweranso mtimu ya Kansas City Current, wasankhidwa kupikitsana nawo mu mphoto ya Ballon d'Or.