19/02/2026
🛎SIMUDZAPHUNZIRA KU SUKULU KOMA NDIZOKAKAMIZIKA PA INU KUZIDZIWA🛎
You can call me Habeeb❤️ and am your admin here at ZonseTV...Mu post iyi tiona zinthu zofunikira kwambiri.
Pali zinthu zambiri zomwe Sitingaphunzire ku school koma timayenera tizidziwe. Zinthu izi munjira ina zimatchedwa Common sense. Wina aliyense mwaife afunika akhale ndi common sense pochita zinthu.
💥-Ngati mwamuyendera munthu kunyumba kwake ndiye akukamba zoti watopa, bas ingonyamukani mupatseni mpata kaya ali pa banja kapena ayi. Dzilemekezeni ndithu.
💥-Muli ndi Munthu yemwe mwakhala naye mukucheza maka mulendo wakuyenderani kapena mwamuyendera, sizoyenera kuyankhulana pa phone mpaka 15, 20, 30 minutes munthuyo atangokhala aayi..use your common sense Zadah. Yankhani phone mukadziwa kuti pali macheza chabe muuzeni munthuyo "Pepani mungaimbenso after 30 minutes?" Kapena "Ndikuimbilani after mphindi 30" common sense 🙏.
💥-Mukuyenda ndi mzanu kaya mbale wanu kumalo a public/mu msika/ mma trading centers or any other places ndiye akuchita manyazi, Sizomufunsa bwanji ukuchita manyazi aaa cheer up, aayi ...kulakwa. musiyeni ingotsekani pakamwa panupo ndipo pangani zomwe mwapitira.
💥-Munthu wakupatsani mphatso ngati ndrama chonde osalandira ndikuwelenga pomwepo aayi. Landiran muthokozeni, mukapita kuseli kapena akapita ndipomwe mudziwelengano. Chimodzimodzinso akakupatsani gift kaya mu box kaya mu gift bag osatsegula pompo unless mutafunsa, Can I open it?..Munthuyo adzakuyankhani and inuyo mudzaona momwe momwe wayankhira komanso facial expression yake. Common sense.
💥-Munthu wina akuyankhula osamudula pakamwa ayi, Musiyeni amalize zomwe akufuna kukamba kenako ndiye mudzimuyankha. Common sense.
💥-Siyani kumuyang'ana munthu kapena anthu mochititsa manyazi. Munthu wakudutsani, kapena muli naye mu restraunt akudya inu basitu muyang'anane..kumutsitsa kumukweza kumupotokola khosi aaayi pilizi. Common sense.
💥-Chonde siyani kumufunsa munthu mafunso oti sathandiza mu nthawi yomwe akudutsa muzowawa. Leta say munthu wabeledwa, inu mmalo momufunsa kuti wabayo walowera kuti kapena tiyeni ku police,,inu mwayamba kumufunsa aaa akubelanidi? koma zakhala bwanji? Mmm really....? ayi siyani izi. Common sense
💥-Munthu wakupangani Kalibu chakudya please observe the kuchuluka kwa chakudya kaye before you join. Or kapena ingolawani bas auzeni muli bwinobwino. Enatu amatha kuona kuti mwini wakeyutu yamuswa ndipo the food is too less koma amapezeka akudya naye mmaka nthongo yomaliza munthu wakalibu kukhala omaliza iiii pilizi. Common sense.
💥-Kwa anthu amzathu omwe mumakonda ma jokes kapena kuti nthabwala...chonde musanapange ma jokes anuwo pangani kaye check kuti malo muliwo anthu ali mu condition yanji, osangofikira ma jokes mkumayembekezera kuti anthu asangalare kapena aseke pomwe sali mu condition yabwino ..sizabwino.
💥-Mukafuna kulavula makamaka pagulu la anthu kapena pa malo apublic please, osamangolavula aayi...pitani kuseli komwe anthu sakuonani kalavuleni kapena find away yoti anthu sadziona zimalovu zanuzo. Chimodzimodzi kuyetsemula try to cover your nose and your mouth incase if anything comes out youre not embaranced.
💥-Anthu ena sadziwa koma lero mudziwe izi, Mukamayasamula nkhope yanu imasintha mmaonekedwe ndipo mmaoneka moOpsa simasewera kotero Make it a habiti to cover your mouth komanso kudzibweza kuti musayatsamule.
💥-Chonde nkhani ya chakudya, ngati mwapakula chakudya mu poto wanu kuika mmbale ndikumadya china mukudya ndipo china chatsalira mu poto muja, ngati mwachilephera mukudyachi chonde osakaphatikiza ndo chomwe chili mpoto chija, keep it aside. Common sense.
All of these are part of your common sense. Mufunika muzidziwe zimenezi ndipo sizitengera digili kapena phi echi dhi😀 aayi.
_________________________
Osaiwala kupanga LIKE...SHARE...COMMENT...
FOLOW👉 Zonse TV