30/03/2025
MWANA WAMENYA AMAI AKE CHIFUKWA CHOMUMANA NDALAMA
M'mayi mukumuona pachinthunziyu dzina lake ndi Moreen Kachingwe, ndipo iye wamenyedwa modesa nkhawa ndimwana wake wazaka zosaposera 24 m'boma la Blantyre ku Machinjiri.
Titafufuza tapeza kuti mayi yu adamukaniza mwana wawo yo ndalama yoti akamwere mowa, m'nyamata yu akuti aka sikoyamba ndipo akhala akumakiya chitseko makiyi ndikumakagwetsera mu dzenje la chimbudzi akamanidwa kalikonse pakhomopo.