11/01/2026
.
Unduna wa zachuma waitana ena mwa makhansala mdziko muno kuti akaperekepo maganizo awo pa ndondomeko ya chuma cha boma cha 2026-2027.
Mmodzi mwa makhansala omwe CCMnews yapeza, ndi a Maloto Chimkombero yemwe ndi khansala wa Kalira Masamba ward m'boma la Ntchisi.
Unduna wa zachuma motsogozedwa ndi nduna ya undunawu, Hon Joseph Mwanamveka akuyenda mzigawo za dziko lino komwe akumakumana ndi akatswiri komanso adindo ochepa chabe kuti apereke maganizo awo pa zomwe akufuna kuti zikhale mu ndodomeko ya chuma cha boma yomwe iyambe kugwila ntchito pa 1 April chaka chino.
Khansala waku Ntchisiyu, yemwenso ndi wapampando wa khonsolo ya Ntchisi, waikidwa mu gulu lomwe likapereke maganizo ake mu mzinda wa Mzuzu mawa lino pa 12 January 2026.
Mwa zina, a Chimkombero ati akapempha undunawu kuti ukweze malipiro amakhansala, kuika ndondomeko yoti makhansala azigula nawo galimoto zopanda msonkho monga momwe amachitira ma MP, komanso kuti ma DC azigulilidwa galimoto yawoyawo akamagwira ntchito.
Pa nkhani yokhudza ndalama zachitukuko za kudera la phungu (CDF), Chimkombero wati akapempha undunawu kuti ukhazikitse ndondomeko zokhwima komanso zopereka mphamvu ku anthu akumudzi kuti azitha kupanga nawo ziganizo ndikulondoloza momwe CDF iziyendera.
Malingana ndi khansala yu, izi zithandiza kuchepetsa chinyengo chomwe chimakhalapo pa ndalama za chitukuko mmadera zomwe pamapeto pake zimaphinja anthu osauka maka achinyamata, amai ndi ana.
Khansala Chimkombero, yemwenso ndi wachiwiri kwa Prezident wa Malawi Local Government Association (MALGA), ndi mmodzi mwa andale achinyamata amene boma likumawafuna pafupipafupi pa zinthu zokhudza dziko lino.
Ndipo mmau ake, Chimkombero wapempha achinyamata kuti asamaope kutenga nawo gawo pa utsogoleri wa ndale m'dziko muno.
Khansala Chimkombero ndi mmodzi mwa makhansala asanu( 5) omwe akakhale nawo ku zokambiranazi.
Wolemba: Tchovaldinho Linyama-Ntchisi (11-01-2026).