11/12/2025
Nkhani za masewera
>Masewera a tennis azimayi akuyembekezeka kukulirakulira, pomwe bungwe la Women's Tennis Association (WTA), ndi kampani yokonza ma galimoto ya Mercedes-Benz, afika pamgwirizano omwe ungathe kuyika ndalama zokwana 500 miliyoni US dollars m'masewerawa kwazaka zopyola khumi. Kampani yodziwika bwinoyi, yopanga magalimoto yamdziko la German, ikuyenera kukhazikitsa mgwirizano ndi bungwe la WTA, ndikutsanulira ndalama pafupifupi 50 miliyoni US dollars pa chaka, mumasewera a tennis azimayi kwa zaka pafupifupi khumi
>Gavi, bungwe limene limawonetsetsa kuti katemera azipezeka m'maiko osauka, limodzi ndi bungwe la Union of European Football Associations (UEFA), agwirizana ndi bungwe la Confederation of African Football (CAF), ndipo anachititsa msonkhano wokhudza kukhulupilira katemera, kwa achinyamata ku sukulu ya Heritage mu mzinda wa Harare mdziko la Zimbabwe dzulo lachitatu, ngati gawo la mpikisano wa atsikana wa Southern Africa's Girls Integrated Football Tournament (GIFT). Pamwambowu, panali atsikana pafupifupi maza awiri azaka pakati pa khumi ndi zinayi, mpaka khumu, zisanu ndi ziwiri, ochokera m'maiko a Malawi, Zimbabwe, Namibia, South Africa, Zambia, ndi Lesotho.
>Hugo Broos, mphunzitsi wamkulu wa timu ya mpira ya amuna yadziko la South Africa, watenga njira yokhwima pankhani ya nkhalidwe mu timu yake, pambuyo pa katswiri osewera kumbuyo kwa timuyo, Mbekezeli Mbokazi, kufika mochedwa pa ntchito yake ndi timu yadzikolo. Mbokazi, amene amaseweranso ndi timu ya Orlando Pirates yamdziko la South Africa, amayenera kufika mumsasa watimuyo lachiwiri, Broos atampatsa tsiku limodzi lowonjezera lopuma kutsatira kupambana kwa Orlando Pirates mpikisano wa Carling Knockout loweluka lapitali. Komabe Mbokazi, omwe ndi wazaka makumi awiri ndi chimodzi, anaphonya tsiku lomaliza ponena kuti anasemphana ndi ndege. Kufika kwake mochedwa kwakhumudwitsa Hugo Broos...…
>Wapampando wa timu yampira wamiyendo ya TS Galaxy yamdziko la South Africa, Tim Sukazi, walozanso chala makampani amdziko la South Africa, kudzudzula makampani akuluakulu, kuti akunyalanyaza timuyo ngakhale ikuchita bwino. Sukazi watchula mosabisa mawu kampani ya First National Bank (FNB), kunena kuti bankiyo yasiya kuthandiza masewera a mpira, timu ya Cape Town City itatulutsidwa mu ligi yayikulu nyengo yatha yamasewera, chifukwa bankiyo sikufuna kukhazikitsa mgwirizano ndi timu ya munthu wachikuda. Ngakhale akuwona kuti ndizolakwika, Sukazi wati timuyo ipitiriza kupita patsogolo…….
>Katswiri wakale watimu yampira wamiyendo yadziko la Zambia, Christopher Katongo, walandila timu yadzikolo kukatenga mbali mumpikisano wa Africa Cup of Nations kachiwiri motsatizana. Katongo, amene anathandiza Zambia kunyamula chikho cha AFCON mchaka cha 2012, wafunira timuyo zabwino zones, koma wati luso lambiri likufinika ngati akufuna kukanyamulanso chikho. Katongo wanenetsa kuti osewera asakapanikizidwe kwambiri patsogolo pa mpikisanowo mdziko la Morocco, komwe Zambia ikakumane ndi Morocco, yomwe ikugwirizira mpikisanowu, Mali, ndi Comoros mu Gulu A.
Alex Nkhuku
Channel Africa News.