16/10/2025
Sad π’ π
Mbali yakuno tadzadzidwa ndi chisoni pakumva za imfa ya Rittah Ekari Nazombe mmawa uno, uyutu ndi mwana oyamba wa malemu O'Brien Nazombe uja anali katswiri wa ndakatuko komanso anazutsa ndakatulo za pawailesi kuzera mu programme ija ya Patsinde pa Joy Radio.
Mtsikana yu wamwalira atangodwala kanthawi kochepa ku chipatala cha Queens ku Blantyre m'bandakucha uno, kwa inu amene simumamudziwa Rittah Ekari Nazombe anali nurse yemwe amagwira ntchito yake ku Lilongwe ππ.
Maliro akalilira ku Machinjiri ku Area 6 komwe ndi kwao kwa Rittah Ekari Nazombe.
RIPποΈποΈποΈποΈποΈποΈ